[27] “Kwezani mbendera ya nkhondo mʼdziko! Lizani lipenga pakati pa mitundu ya anthu! Konzekeretsani mitundu ya anthu kuti ikamuthire nkhondo; itanani maufumu awa: Ararati, Mini ndi Asikenazi kuti adzamuthire nkhondo. Ikani mtsogoleri wankhondo kuti amenyane naye; tumizani akavalo ochuluka ngati magulu a dzombe.